×

chikulupi cha uislamu (Chichewa)

Preparation: Sheikh Muhammadi Abdul-Hamid Silika

Description

Ndithu matamando onse ndi a Allah, tikumutamanda, kumpempha chithandizo ndi kumpempha chikhululuko, komanso tikuzichinjiriza mwa Allah ku zoyipa za mitima ndi ntchito zathu. Amene Allah wamuongola palibe angamusocheretse, ndipo amene wasochera palibe angamuongole. Ndikuchitira umboni kuti palibe mulungu wina (woyenera kupembedzedwa) koma Allah, Wayekha, wopanda wothandizana naye. Ndikuchitiranso umboni kuti Muhammadi  ndikapolo wake komanso mtumiki wake. Adamtumidza ndi chiongoko kudzanso chipembedzo chowona kuti achiyike pamwamba pa zipembedzo zonse ngakhale opembedza mafano ziwanyanse. Pambuyo pa izi: Uku ndiko kutsindikiza koyamba kwa buku la Chikhulupiriro cha Chisilamu, lomwe ndikulipereka kwa anthu a dziko lonse. Buku limeneli ndi zipatso za mapologalamu a Tauhidi omwe ndakhala ndikulalika pa Radio Islam kwa zaka zambiri. Ndipo ndaligawa magawo awiri. Mu gawo loyamba ndakambamo za Tauhidi mmene iliri mu Qur’an ndi Sunnah. Posonkhanitsa ziphunzitso zake ndayazamira buku la Aqidah lomwe lidalembedwa ndi gulu la masheikh omwe ndi akadaulo pa maphunziro a Tauhidi ochokera pa sukulu ya ukachenjede ya Chisilamu ya ku Madinatu Munawwara, komanso sukulu ya ukachenjede ya Chisilamu ya Imam Muhammadi Ibn Saudi mdziko la Saudi Arabia. Mu gawo lachiwiri ndakambamo za Tauhidi mmene iliri mu Baibulo. Posonkhanitsa ziphunzitso zake ndayazamira buku la Mukhtaŝar Kitāb Iđ’hār Al-Haqq lomwe lidalembedwa ndi Sheikh Rahmatu Allah Al-Hindi (Allah awachitire chifundo). Pali masheikh omwe awunika bukuli ndi kuvomereza kuti liri bwino. Iwo ndi: Sheikh Ahmad Chienda, Sheikh Omar Adam Nkachelenga, Sheikh Faruq Jum’a Chibaya ndi Sheikh Dr. Salmin Omar Idrus. Sheikh Muhammadi Abdul-Hamid Silika Al-Madani

Download Book

معلومات المادة باللغة العربية