×

QUR’AN YOLEMEKEZEKA yotanthauzidwa m’chichewa (Chichewa)

Description

Chifukwa chakufunika kwa uthengawu kuti ufike kwa anthu onse, a Bungwe la Africa Muslim Agency adandipempha kuti ndimasulire Qur’an m’chichewa, ndicholinga chakuti amene sangathe kumvetsa uthenga wake m’chiarabu, aumve m’chilankhulo chawo cha Chichewa. Choncho ntchitoyi idagwirikadi kotero kuti munthu akawerenga bwinobwino akhoza kumva uthenga wa Mulungu m’Qur’an. Ndayetsetsa m’kutanthauzira kwanga mawu oyerawa kuti musakhale zolakwika zambiri, koma ntchito yogwira Munthu siilephera kupezeka zolakwika kupatula zochita za Chauta. Munthu ndi Munthu basi. Choncho ndikupempha aliyense amene angapeze zolakwika pakatanthauzidwe ka Qur’an kapena kasankhidwe kamawu oyerawa, kuti anditumizire ndi cholinga choti pomazatuluka bukuli kachiwiri muzakhale mopanda zolakwika zimenezo. Pamene ndimagwira ntchitoyi, panali mabuku amene ndimathandizika nawo pakasankhidwe ka kutanthauzira koyenera kwa Qur’an, komanso anthu amene amandithandiza pakasankhidwe ka mawu oyenera m’chichewa. Mabukuwa ndi awa Tafsiri ya Jalalain, Tafsiri ya ibn Kathiri, Al Muntakhab ndi Swafuat Tafaasiri. Ndipo Ntchito yotanthauzira inatha m’chaka cha 1987 pambuyo poigwira mzaka zitatu. Ndipo kuyambira nthawiyo kufikana m’chaka cha 1999 yakhala ikuunikidwa ndi ma Sheikh akuluakulu m’dziko muno. Ine M’bale Wanu -Sheikh Khalid Ibrahim

Download Book

معلومات المادة باللغة العربية